bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.13 kB
JSON
["Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;ndisungeni kwa munthu wachiwawa;","amene adzipanga zoipa mumtima mwao;masiku onse amemeza nkhondo.","Anola lilime lao ngati njoka;pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.","Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa;ndisungeni kwa munthu wachiwawa;kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.","Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe;anatcha ukonde m'mphepete mwa njira;ananditchera makwekwe.","Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.","Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa,munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.","Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze.","Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,choipa cha milomo yao chiwaphimbe.","Makala amoto awagwere;aponyedwe kumoto;m'maenje ozama, kuti asaukenso.","Munthu wamlomo sadzakhazikika pa dziko lapansi;choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.","Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu,ndi kuweruzira aumphawi.","Indedi, olungama adzayamika dzina lanu;oongoka mtima adzakhala pamaso panu."]