bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 683 B
JSON
["Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu.Achita zovunda, achita ntchito zonyansa;kulibe wakuchita bwino.","Yehova m'Mwamba anaweramira pa ana a anthu,kuti aone ngati aliko wanzeru,wakufuna Mulungu.","Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima;palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.","Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu?Pakudya anthu anga monga akudya mkate,ndipo saitana pa Yehova.","Pamenepa anaopaopatu,pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.","Munyazitsa uphungu wa wozunzika,koma Yehova ndiye pothawira pake.","Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni!Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga,pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele."]