bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 863 B
JSON
["Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse;ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.","Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera,ndi kuyamika dzina lanu,chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu;popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.","Tsiku loitana ine, munandiyankha,munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.","Mafumu onse a pa dziko lapansi adzakuyamikani,Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.","Ndipo adzaimbira njira za Yehova;pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.","Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;koma wodzikuza amdziwira kutali.","Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.","Yehova adzanditsirizira za kwa ine:Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse:Musasiye ntchito za manja anu."]