UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.67 kB
["Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova!Lemekezani inu atumiki a Yehova.","Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova,m'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.","Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino;muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.","Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo,Israele, akhale chuma chake chenicheni.","Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu,ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.","Chilichonse chimkonda Yehova achichita,kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.","Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi;ang'animitsa mphezi zidzetse mvula;atulutsa mphepo mosungira mwake.","Anapanda oyamba a Ejipito,kuyambira munthu kufikira zoweta.","Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe,pa Farao ndi pa omtumikira onse.","Ndiye amene anapanda amitundu ambiri,napha mafumu amphamvu;","Sihoni mfumu ya Aamori,ndi Ogi mfumu ya Basani,ndi maufumu onse a Kanani:","Ndipo anapereka dziko lao likhale chosiyira,chosiyira cha kwa Israele anthu ake.","Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo.","Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,koma adzaleka atumiki ake.","Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide,ntchito ya manja a anthu.","Pakamwa ali napo koma osalankhula;maso ali nao, koma osapenya;","makutu ali nao, koma osamva;inde, pakamwa pao palibe mpweya.","Akuwapanga adzafanana nao;inde, onse akuwakhulupirira.","A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova:A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova:","A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova:Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova.","Alemekezedwe Yehova kuchokera m'Ziyoni,amene akhala m'Yerusalemu.Aleluya."]