UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.39 kB
["Yehova, kumbukirani Davidekuzunzika kwake konse.","Kuti analumbira Yehova,nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,","Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga,ngati ndidzakwera pa kama logonapo;","ngati ndidzalola maso anga agone,kapena zikope zanga ziodzere;","kufikira nditapezera Yehova malo,chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?","Taonani, tinachimva m'Efurata;tinachipeza kuchidikha cha kunkhalango.","Tidzalowa mokhalamo Iye;tidzagwadira kumpando wa mapazi ake.","Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu.","Ansembe anu avale chilungamo;ndi okondedwa anu afuule mokondwera.","Chifukwa cha Davide mtumiki wanumusabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.","Yehova analumbira Davide zoona;sadzalibweza; ndi kuti,Wa iwo okhala zipatso za thupi lakondidzaika pa mpando wachifumu wako.","Ana ako akasunga chipangano changandi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa,ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse,","pakuti Yehova anasankha Ziyoni;analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti,","Pampumulo panga mpano posatha,Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.","Ndidzadalitsatu chakudya chake;aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate.","Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso:Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera.","Apo ndidzaphukitsira Davide nyanga;ndakonzeratu wodzozedwa wanga nyali.","Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi;koma pa iyeyu korona wake adzamveka."]