bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 13.1 kB
JSON
["Odala angwiro m'mayendedwe ao,akuyenda m'chilamulo cha Yehova.","Odala iwo akusunga mboni zake,akumfuna ndi mtima wonse;","inde, sachita chosalungama;ayenda m'njira zake.","Inu munatilamulira,tisamalire malangizo anu ndi changu.","Ha? Mwenzi zitakhazikika njira zangakuti ndisamalire malemba anu.","Pamenepo sindidzachita manyazi,pakupenyerera malamulo anu onse.","Ndidzakuyamikani ndi mtima woongoka,pakuphunzira maweruzo anu olungama.","Ndidzasamalira malemba anu:Musandisiye ndithu.","Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?Akawasamalira monga mwa mau anu.","Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse;ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.","Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga,kuti ndisalakwire Inu.","Inu ndinu wodala Yehova;ndiphunzitseni malemba anu.","Ndinafotokozera ndi milomo yangamaweruzo onse a pakamwa panu.","Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu,koposa ndi chuma chonse.","Ndidzalingirira pa malangizo anu,ndi kupenyerera mayendedwe anu.","Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;sindidzaiwala mau anu.","Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;ndipo ndidzasamalira mau anu.","Munditsegulire maso, kuti ndipenyezodabwitsa za m'chilamulo chanu.","Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;musandibisire malamulo anu.","Mtima wanga wasweka ndi kukhumbamaweruzo anu nyengo zonse.","Munadzudzula odzikuza otembereredwa,iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.","Mundichotsere chotonza, ndi chimpepulo;pakuti ndinasunga mboni zanu.","Nduna zomwe zinakhala zondineneza;koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.","Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa,ndizo zondipangira nzeru.","Moyo wanga umamatika ndi fumbi;mundipatse moyo monga mwa mau anu.","Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha:Mundiphunzitse malemba anu.","Mundizindikiritse njira ya malangizo anu;kuti ndilingalire zodabwitsa zanu.","Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni:Mundilimbitse monga mwa mau anu.","Mundichotsere njira ya chinyengo;nimundipatse mwachifundo chilamulo chanu.","Ndinasankha njira yokhulupirika;ndinaika maweruzo anu pamaso panga.","Ndimamatika nazo mboni zanu;musandichititse manyazi, Yehova.","Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,mutakulitsa mtima wanga.","Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;ndidzaisunga kufikira kutha kwake.","Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu;ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.","Mundiyendetse mopita malamulo anu;pakuti ndikondwera m'menemo.","Lingitsani mtima wanga kumboni zanu,si ku chisiriro ai.","Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe,mundipatse moyo mu njira yanu.","Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,ndiye wodzipereka kukuopani.","Mundipatutsire chotonza changa ndichiopacho;popeza maweruzo anu ndi okoma.","Taonani, ndinalira malangizo anu;mundipatse moyo mwa chilungamo chanu.","Ndipo chifundo chanu chindidzere, Yehova,ndi chipulumutso chanu, monga mwa mau anu.","Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;popeza ndikhulupirira mau anu.","Ndipo musandichotsere ndithu mau a choonadi pakamwa panga;pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.","Potero ndidzasamalira malamulo anu chisamalirekunthawi za nthawi.","Ndipo ndidzayenda mwaufulu;popeza ndinafuna malangizo anu.","Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,osachitapo manyazi.","Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu,amene ndiwakonda.","Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda;ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.","Kumbukirani mau a kwa mtumiki wanu,amene munandiyembekezetsa nao.","Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi;pakuti mau anu anandipatsa moyo.","Odzikuza anandinyoza kwambiri:koma sindinapatukanso nacho chilamulo chanu.","Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova,ndipo ndinadzitonthoza.","Ndinasumwa kwakukulu,chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu.","Malemba anu anakhala nyimbo zangam'nyumba ya ulendo wanga.","Usiku ndinakumbukira dzina lanu, Yehova,ndipo ndinasamalira chilamulo chanu.","Ichi ndinali nacho,popeza ndinasunga malangizo anu.","Yehova ndiye gawo langa:Ndinati ndidzasunga mau anu.","Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse:Mundichitire chifundo monga mwa mau anu.","Ndinaganizira njira zanga,ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.","Ndinafulumira, osachedwa,kusamalira malamulo anu.","Anandikulunga nazo zingwe za oipa;koma sindinaiwala chilamulo chanu.","Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikanichifukwa cha maweruzo anu olungama.","Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani,ndi iwo akusamalira malangizo anu.","Dziko lapansi lidzala nacho chifundo chanu, Yehova;mundiphunzitse malemba anu.","Munachitira mtumiki wanu chokoma, Yehova,monga mwa mau anu.","Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru;pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.","Ndisanazunzidwe ndinasokera;koma tsopano ndisamalira mau anu.","Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino;mundiphunzitse malemba anu.","Odzikuza anandipangira bodza:Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.","Mtima wao unona ngati mafuta;koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.","Kundikomera kuti ndinazunzidwa;kuti ndiphunzire malemba anu.","Chilamulo cha pakamwa panu chindikomerakoposa golide ndi siliva zikwizikwi.","Manja anu anandilenga nandiumba;mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.","Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera;popeza ndayembekezera mau anu.","Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova,ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.","Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani,monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.","Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo;popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.","Odzikuza achite manyazi, popeza anandichitira monyenga ndi bodza:Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.","Iwo akuopa Inu abwere kwa ine,ndipo adzadziwa mboni zanu.","Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu;kuti ndisachite manyazi.","Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu:Ndinayembekezera mau anu.","Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,ndikuti, Mudzanditonthoza liti?","Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;koma sindiiwala malemba anu.","Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?","Odzikuza anandikumbira mbuna,ndiwo osasamalira chilamulo chanu.","Malamulo anu onse ngokhulupirika;andilondola nalo bodza; ndithandizeni.","Akadandithera pa dziko lapansi;koma ine sindinasiya malangizo anu.","Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu;ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.","Mau anu aikika kumwamba,kosatha, Yehova.","Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo;munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.","Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero;pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.","Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa,ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.","Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse;popeza munandipatsa nao moyo.","Ine ndine wanu, ndipulumutsenipakuti ndinafuna malangizo anu.","Oipa anandilalira kundiononga;koma ndizindikira mboni zanu.","Ndinapenya malekezero ake a ungwiro wonse;koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.","Ha! Ndikondadi chilamulo chanu;ndilingiriramo ine tsiku lonse.","Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga;pakuti akhala nane chikhalire.","Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse;pakuti ndilingalira mboni zanu.","Ndizindikira koposa okalambapopeza ndinasunga malangizo anu.","Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa,kuti ndisamalire mau anu.","Sindinapatukana nao maweruzo anu;pakuti Inu munandiphunzitsa.","Mau anu azunadi powalawa ine!Koposa uchi m'kamwa mwanga.","Malangizo anu andizindikiritsa;chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.","Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga,ndi kuunika kwa panjira panga.","Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima,kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.","Ndazunzika kwambiri:Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.","Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga,ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.","Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire;koma sindiiwala chilamulo chanu.","Oipa ananditchera msampha;koma sindinasokera m'malangizo anu.","Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha;pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.","Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu,kosatha, kufikira chimaliziro.","Ndidana nao a mitima iwiri;koma ndikonda chilamulo chanu.","Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa;ndiyembekezera mau anu.","Mundichokere ochita zoipa inu;kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.","Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo;ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa.","Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa,ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire.","Mupepula onse akusokera m'malemba anu;popeza chinyengo chao ndi bodza.","Muchotsa oipa onse a pa dziko lapansi ngati mphala:Chifukwa chake ndikonda mboni zanu.","Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu;ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.","Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo;musandisiyira akundisautsa.","Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere;odzikuza asandisautse.","Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu,ndi mau a chilungamo chanu.","Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu,ndipo ndiphunzitseni malemba anu.","Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni;kuti ndidziwe mboni zanu.","Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu;pakuti anaswa chilamulo chanu.","Chifukwa chake ndikonda malamulo anukoposa golide, inde golide woyengeka.","Chifukwa chake ndiyesa ngolunjikamalangizo anu onse akunena zonse;koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.","Mboni zanu nzodabwitsa;chifukwa chake moyo wanga uzisunga.","Potsegulira mau anu paunikira;kuzindikiritsa opusa.","Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu;popeza ndinakhumba malamulo anu.","Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo,monga mumatero nao akukonda dzina lanu.","Khazikitsani mapazi anga m'mau anu;ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse.","Mundiombole kunsautso ya munthu:Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.","Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu;ndipo mundiphunzitse malemba anu.","Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi,popeza sasamalira chilamulo chanu.","Inu ndinu wolungama, Yehova,ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.","Mboni zanuzo mudazilamulirazili zolungama ndi zokhulupirika ndithu.","Changu changa chinandithera,popeza akundisautsa anaiwala mau anu.","Mau anu ngoyera ndithu;ndi mtumiki wanu awakonda.","Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa;koma sindiiwala malemba anu.","Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha;ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.","Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.","Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.","Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;ndidzasunga malemba anu.","Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,ndipo ndidzasamalira mboni zanu.","Ndinafuula kusanake:ndinayembekezera mau anu.","Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku,kuti ndilingirire mau anu.","Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu;mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.","Otsata zachiwembu andiyandikira;akhala kutali ndi chilamulo chanu.","Inu muli pafupi, Yehova;ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi.","Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu,kuti munazikhazika kosatha,","Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;pakuti sindiiwala chilamulo chanu.","Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;mundipatse moyo monga mwa mau anu.","Chipulumutso chitalikira oipa;popeza safuna malemba anu.","Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova;mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.","Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri;koma sindinapatukana nazo mboni zanu.","Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;popeza sasamalira mau anu.","Penyani kuti ndikonda malangizo anu;mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu.","Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi;ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.","Nduna zinandilondola kopanda chifukwa;koma mtima wanga uchita mantha nao mau anu.","Ndikondwera nao mau anu,ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.","Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo;koma ndikonda chilamulo chanu.","Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,chifukwa cha maweruzo anu alungama.","Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri;ndipo alibe chokhumudwitsa.","Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova,ndipo ndinachita malamulo anu.","Moyo wanga unasamalira mboni zanu;ndipo ndizikonda kwambiri.","Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu;popeza njira zanga zonse zili pamaso panu.","Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova;mundizindikiritse monga mwa mau anu.","Kupemba kwanga kudze pamaso panu;mundilanditse monga mwa mau anu.","Milomo yanga itulutse chilemekezo;popeza mundiphunzitsa malemba anu.","Lilime langa liimbire mau anu;pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.","Dzanja lanu likhale lakundithandiza;popeza ndinasankha malangizo anu.","Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova;ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.","Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani;ndipo maweruzo anu andithandize.","Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu;pakuti sindiiwala malamulo anu."]