bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.14 kB
JSON
["Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;pakuti chifundo chake nchosatha.","Anene tsono Israele,kuti chifundo chake nchosatha.","Anene tsono nyumba ya Aroni,kuti chifundo chake nchosatha.","Anene tsono iwo akuopa Yehova,kuti chifundo chake nchosatha.","M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.","Yehova ndi wanga; sindidzaopa;adzandichitanji munthu?","Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.","Kuthawira kwa Yehova nkokomakoposa kukhulupirira munthu.","Kuthawira kwa Yehova nkokomakoposa kukhulupirira akulu.","Amitundu onse adandizinga,zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.","Adandizinga, inde, adandizinga:Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.","Adandizinga ngati njuchi;anazima ngati moto waminga;indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.","Kundikankha anandikankha ndikadagwa;koma Yehova anandithandiza.","Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;ndipo anakhala chipulumutso changa.","M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondweraDzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:","Dzanja lamanja la Yehova likwezeka,Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu.","Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.","Kulanga anandilangadi Yehova:koma sanandipereke kuimfa ai.","Nditsegulireni zipata za chilungamo;ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.","Chipata cha Yehova ndi ichi;olungama adzalowamo.","Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,ndipo munakhala chipulumutso changa.","Mwala umene omangawo anaukanawakhala mutu wa pangodya.","Ichi chidzera kwa Yehova;nchodabwitsa ichi pamaso pathu.","Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.","Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.","Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova;takudalitsani kochokera m'nyumba ya Yehova.","Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.","Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.","Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino,pakuti chifundo chake nchosatha."]