UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.42 kB
["Ndimkonda, popeza Yehova amamvamau anga ndi kupemba kwanga.","Popeza amanditcherera khutu lake,chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse.","Zingwe za imfa zinandizinga,ndi zowawa za manda zinandigwira:ndinapeza nsautso ndi chisoni.","Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova;ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.","Yehova ngwa chifundo ndi wolungama;ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.","Yehova asunga opusa;ndidafooka ine, koma anandipulumutsa.","Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako;pakuti Yehova anakuchitira chokoma.","Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa,maso anga kumisozi,mapazi anga, ndingagwe.","Ndidzayenda pamaso pa Yehovam'dziko la amoyo.","Ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula;ndinazunzika kwambiri.","Pofulumizidwa mtima ndinati ine,anthu onse nga mabodza.","Ndidzabwezera Yehova chiyanichifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?","Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso,ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.","Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova,tsopano, pamaso pa anthu ake onse.","Imfa ya okondedwa akenja mtengo wake pamaso pa Yehova.","Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu;ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;mwandimasulira zondimanga.","Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko,ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.","Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova,tsopano, pamaso pa anthu ake onse.","M'mabwalo a nyumba ya Yehova,pakati pa inu, Yerusalemu.Aleluya."]