UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.31 kB
["Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai,koma kwa dzina lanu patsani ulemerero,chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.","Aneneranji amitundu,Ali kuti Mulungu wao?","Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba;achita chilichonse chimkonda.","Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide,ntchito za manja a anthu.","Pakamwa ali napo, koma osalankhula;maso ali nao, koma osapenya;","makutu ali nao, koma osamva;mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;","manja ali nao, koma osagwira;mapazi ali nao, koma osayenda;kapena sanena pammero pao.","Adzafanana nao iwo akuwapanga;ndi onse akuwakhulupirira.","Israele, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.","Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao, ndi chikopa chao.","Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova;ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.","Yehova watikumbukira; adzatidalitsa:adzadalitsa nyumba ya Israele;adzadalitsa nyumba ya Aroni.","Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,aang'ono ndi aakulu.","Yehova akuonjezereni dalitso,inu ndi ana anu.","Odalitsika inu a kwa Yehova,wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.","Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova;koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.","Akufa salemekeza Yehova,kapena aliyense wakutsikira kuli chete:","Koma ife tidzalemekeza Yehovakuyambira tsopano kufikira nthawi yonse.Aleluya."]