bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 877 B
JSON
["Aleluya.Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse,mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.","Ntchito za Yehova nzazikulu,zofunika ndi onse akukondwera nazo.","Chochita Iye ncha ulemu, ndi ukulu:Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha.","Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake;Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.","Anapatsa akumuopa Iye chakudya;adzakumbukira chipangano chake kosatha.","Anaonetsera anthu ake mphamvu ya ntchito zake,pakuwapatsa cholowa cha amitundu.","Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo;malangizo ake onse ndiwo okhulupirika.","Achirikizika kunthawi za nthawi,achitika m'choonadi ndi chilunjiko.","Anatumizira anthu ake chipulumutso;analamulira chipangano chake kosatha;dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.","Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru;onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma;chilemekezo chake chikhalitsa kosatha."]