UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.25 kB
["Yehova, imvani pemphero langa,ndipo mfuu wanga ufikire Inu.","Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga;munditchereze khutu lanu;tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.","Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi,ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.","Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota;popeza ndiiwala kudya mkate wanga.","Chifukwa cha liu la kubuula kwangamnofu wanga umamatika kumafupa anga.","Ndikunga vuwo m'chipululu;ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.","Ndidikira, ndikhala ngati mbalameili yokha pamwamba pa tsindwi.","Adani anga anditonza tsiku lonse;akundiyalukirawo alumbirira ine.","Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,ndi kusanganiza chomwera changa ndi misozi,","chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu;popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.","Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali;ndipo ine ndauma ngati udzu.","Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse;ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo.","Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni;popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.","Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yake,nachitira chifundo fumbi lake.","Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova,ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.","Pakuti Yehova anamanga Ziyoni,anaoneka m'ulemerero wake;","anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,osapepula pemphero lao.","Ichi adzachilembera mbadwo ukudza;ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.","Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ake opatulika;Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;","kuti amve kubuula kwa wandende;namasule ana a imfa.","Kuti anthu alalikire dzina la Yehova m'Ziyoni,ndi chilemekezo chake m'Yerusalemu;","Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,ndi maufumu kuti atumikire Yehova.","Iye analanda mphamvu yanga panjira;anachepsa masiku anga.","Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga:Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo.","Munakhazika dziko lapansi kalelo;ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu.","Zidzatha izi, koma Inu mukhala:Inde, zidzatha zonse ngati chovala;mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:","Koma Inu ndinu yemweyo,ndi zaka zanu sizifikira kutha.","Ana a atumiki anu adzakhalitsa,ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu."]