bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.62 kB
JSON
["Muimiranji patali, Yehova?Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?","Podzikuza woipa apsereza waumphawi;agwe m'chiwembu anapanganacho.","Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake,adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.","Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira.Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.","Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse;maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;adani ake onse awanyodola.","Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine;ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine.","M'kamwa mwake mwadzala kutembererandi manyengo ndi kuchenjerera;pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.","Akhala m'molalira midzi;mobisalamo akupha munthu wosachimwa.Ambisira waumphawi nkhope yake.","Alalira monga mkango m'ngaka mwake;alalira kugwira wozunzika,agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwake.","Aunthama, nawerama,ndipo aumphawi agwa m'zala zake.","Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala;wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.","Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;musaiwale ozunzika.","Woipa anyozeranji Mulungu,anena m'mtima mwake, Simudzafunsira?","Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitsondi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu;waumphawi adzipereka kwa Inu;wamasiye mumakhala mthandizi wake.","Thyolani mkono wa woipa;ndipo wochimwa, mutsate choipa chakekufikira simuchipezanso china.","Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya;aonongeka amitundu m'dziko lake.","Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika,mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;","kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa."]