bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 998 B
JSON
["Koma Yobu anayankha, nati,","Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu.Kulipulumutsa dzanja losalimba!","Wampangira bwanji wopanda nzeruyu!Ndi kudziwitsa nzeru zenizeni mochuluka!","Wafotokozera yani mau?Ndi mzimu wa yani unatuluka mwa iwe?","Adafawo anjenjemerapansi pa madzi ndi zokhalamo.","Kumanda kuli padagu pamaso pake,ndi kuchionongeko kusowa chophimbako.","Ayala kumpoto popanda kanthu,nalenjeka dziko pachabe.","Amanga madzi m'mitambo yake yochindikira;ndi mtambo sung'ambika pansi pake.","Atchingira pa mpando wake wachifumu,nayalapo mtambo wake.","Analembera madziwo malire,mpaka polekeza kuunika ndi mdima.","Mizati ya thambo injenjemera,ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.","Mwa mphamvu yake agwetsa nyanja bata;ndipo mwa luntha lake akantha kudzikuza kwake.","Mwa mzimu wake anyezimiritsa thambo;dzanja lake linapyoza njoka yothawayo.","Taonani, awa ndi malekezero a njira zake;ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono;koma kugunda kwa mphamvu yake akudzindikiritsa ndani?"]