bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.16 kB
JSON
["Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo?Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?","Alipo akusendeza malire;alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.","Akankhizira kwao bulu wa amasiye,atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale chikole.","Apatukitsa aumphawi m'njira;osauka a padziko abisala pamodzi.","Taonani, ngati mbidzi za m'chipululuatulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya;chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao.","Atema dzinthu zao m'munda;natola khunkha m'munda wampesa wa woipa.","Agona amaliseche usiku wonse opanda chovala,alibe chofunda pachisanu.","Avumbwa ndi mvula kumapiri,nafukata thanthwe posowa pousapo.","Akwatula wamasiye kubere,natenga chikole chovala cha osauka;","momwemo ayenda amaliseche opanda chovala,nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.","M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.","M'mudzi waukulu anthu abuula alinkufa;ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula;koma Mulungu sasamalira choipacho.","Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,sadziwa njira zake, Sasunga mayendedwe ake.","Kukacha auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;ndi usiku asanduka mbala.","Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira,ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;navala chophimba pankhope pake.","Kuli mdima aboola nyumba,usana adzitsekera,osadziwa kuunika.","Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa;pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.","Atengedwa ngati choyandama pamadzi;gawo lao litembereredwa padziko;sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa.","Chilala ndi dzuwa zitha madzi a chipale chofewa,momwemo manda achita nao ochimwa.","M'mimba mudzamuiwala;mphutsi zidzamudya mokondwera.Sadzamkumbukiranso;ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo.","Alusira chumba wosabala,osamchitira wamasiye chokoma.","Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yake;iwo aukanso m'mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo.","Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo;koma maso ake ali pa njira zao.","Akwezeka; m'kamphindi kuli zii;inde atsitsidwa, achotsedwa monga onse ena,adulidwa ngati tirigu ngala zake.","Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza,ndi kuyesa mau anga opanda pake?"]