UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.36 kB
["Koma Yobu anayankha, nati,","Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwake.","Ha! Ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,kuti ndifike kumpando wake!","Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pake,ndikadadzaza m'kamwa mwanga ndi matsutsano.","Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,ndikadazindikira chimene akadanena nane.","Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yake yaikulu?Iai, koma akadanditcherera khutu.","Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;ndipo ndikadapulumuka chipulumukire kwa Woweruza wanga.","Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye;kapena m'mbuyo sindimzindikira;","akachita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;akabisala kulamanja, sindimuona.","Koma adziwa njira ndilowayi;atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.","Phazi langa lagwiratu moponda Iye,ndasunga njira yake, wosapatukamo.","Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake;ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.","Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.","Pakuti adzachita chondiikidwiratu;ndipo zambiri zotere zili ndi Iye.","Chifukwa chake ndiopsedwa pankhope pake;ndikalingirira, ndichita mantha ndi Iye.","Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.","Popeza sindinalikhidwa usanafike mdimawo,ndipo sanandiphimbire nkhope yanga ndi mdima wa bii."]