bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.3 kB
JSON
["Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika,kumanda kwandikonzekeratu.","Zoonadi, ali nane ondiseka;ndi diso langa lili chipenyere m'kundiwindula kwao.","Mupatse chigwiriro tsono,mundikhalire chikole Inu nokha kwanu;ndani adzapangana nane kundilipirira?","Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;chifukwa chake simudzawakuza.","Iye wakupereka mabwenzi ake ku ukapolo,m'maso mwa ana ake mudzada.","Anandiyesanso nthanthi za anthu;ndipo ndakhala ngati munthu womthira malovu pankhope pake.","M'diso mwanga muchita chizirezire chifukwa cha chisoni,ndi ziwalo zanga zonse zilibe chithunzi.","Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho,ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo.","Koma wolungama asungitsa njira yake,ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.","Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.","Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,zakezake zomwe za mtima wanga.","Zisanduliza usiku ukhale usana;kuunika kuyandikana ndi mdima.","Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga;ndikayala pogona panga mumdima.","Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga;kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;","chilikuti chiyembekezo changa?Inde, chiyembekezo changa adzachiona ndani?","Chidzatsikira kumipingiridzo ya kumanda,pamene tipumulira pamodzi kufumbi."]