UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.87 kB
["Pamenepo Yobu anayankha, nati,","Zoonadi inu ndinu anthu,ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.","Koma inenso ndili nayo nzeru monga inu.Sindingakuchepereni;ndani sadziwa zonga izi?","Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake,ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;munthu wolungama wangwiro asekedwa.","Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwake,limlindira woterereka mapazi ake.","Mahema a achifwamba akhala mumtendere,ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima;amene Mulungu amadzazira dzanja lao.","Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza.","Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza;ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera.","Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse;kuti dzanja la Yehova lichita ichi?","M'dzanja mwake muli mpweya wa zamoyo zonse,ndi mzimu wa munthu aliyense.","M'khutumu simuyesa mau,monga m'kamwa mulawa chakudya chake?","Kwa okalamba kuli nzeru,ndi kwa a masiku ochuluka luntha.","Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu;uphungu ndi luntha ali nazo.","Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso;amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira.","Taona atsekera madzi, naphwa;awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.","Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru.Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ake.","Apita nao maphungu atawafunkhira,napulukiritsa oweruza milandu.","Amasula chomangira cha mafumu,nawamangira nsinga m'chuuno mwao.","Apita nao, ansembe atawafunkhira,nagubuduza amphamvu.","Amchotsera wokhulupirika kunena kwake.Nalanda luntha la akulu.","Atsanulira mnyozo pa akalonga,nawansezera olimba lamba lao.","Avumbulutsa zozama mumdima,natulutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;","achulukitsa amitundu, nawaononganso;abalalikitsa amitundu, nawabwezanso.","Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao,nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira.","Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika,ndipo awayendetsa dzandidzandi."]