UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 3.69 kB
["Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu.","Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawachotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israele.","Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wake, nautsira Abaala maguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.","Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, M'Yerusalemu mudzakhala dzina langa kunthawi zonse.","Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.","Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.","Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse;","ndipo sindidzasunthanso phazi la Israele kudziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kuchita zonse ndawalamulira, chilamulo chonse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose.","Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israele.","Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ake, koma sanasamalire.","Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni.","Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.","Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wake. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.","Chitatha ichi tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa chipata chansomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda.","Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.","Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israele.","Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao.","Machitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israele, taonani, zalembedwa m'machitidwe a mafumu a Israele.","Pemphero lake lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.","Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.","Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri.","Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira Manase atate wake; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate wake, nawatumikira.","Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake.","Ndipo anyamata ake anampangira chiwembu, namupha m'nyumba yakeyake.","Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira chiwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wake akhale mfumu m'malo mwake."]