bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.27 kB
JSON
["Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.","Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adachitira atate wake Uziya; pokhapo sanalowe m'Kachisi wa Yehova. Koma anthu anachitabe zovunda.","Anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofele anamanga kwakukulu.","Namanga midzi m'mapiri a Yuda, ndi m'nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.","Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe.","Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.","Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zake zonse, ndi njira zake, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda.","Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi.","Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ake, namuika m'mudzi wa Davide; ndi Ahazi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake."]