bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 3.64 kB
JSON
["Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.","Iye anamanga Eloti, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.","Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.","Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.","Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza;","popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.","Ndipo Mulungu anamthandiza poyambana ndi Afilisti, ndi Aarabu okhala m'Guribaala, ndi Ameuni.","Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lake linabuka mpaka polowera ku Ejipito; pakuti analimbika chilimbikire.","Uziya anamanganso nsanja m'Yerusalemu pa chipata cha kungodya, ndi pa chipata cha kuchigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.","Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.","Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, otuluka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeiyele, ndi kapitao Maaseiya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.","Chiwerengo chonse cha akulu a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndicho zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi.","Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ochita nkhondo ndi mphamvu yaikulu, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.","Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zachitsulo, ndi malaya achitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera.","Napanga m'Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungodya, aponye nao mivi ndi miyala yaikulu. Ndi dzina lake linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwitsa, mpaka analimbikatu.","Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa m'Kachisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la chofukiza.","Ndipo Azariya wansembe analowa pambuyo pake, ndi pamodzi naye ansembe a Yehova makumi asanu ndi atatu, ndiwo olimba mtima;","natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; tulukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.","Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza ili m'dzanja lake kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe, khate linabuka pamphumi pake, pamaso pa ansembe m'nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo.","Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pake namkankhira msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kutulukako, pakuti Yehova adamkantha.","Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.","Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amozi.","Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake."]