UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 3.01 kB
["Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.","Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele.","Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikulu, zasiliva, ndi zagolide, ndi za mtengo wake, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wake woyamba.","Atauka tsono Yehoramu m'ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.","Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.","Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.","Koma Yehova sanafune kuononga nyumba ya Davide chifukwa cha pangano adalichita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ake nyali nthawi zonse.","Masiku ake Aedomu anapanduka kuchoka m'dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu.","Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ake, ndi magaleta ake onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magaleta.","Chinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lake; chifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.","Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala m'Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.","Ndipo anamdzera kalata wofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayenda m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda,","koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;","taonani, Yehova adzakantha anthu anu, ndi ana anu, ndi akazi anu, ndi chuma chanu chonse, makanthidwe akulu;","ndipo mudzadwala kwakukulu nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzatuluka chifukwa cha nthendayi tsiku ndi tsiku.","Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;","ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Yehowahazi yekha mwana wake wamng'ono.","Ndi pambuyo pake pa izi zonse Yehova anamdwalitsa m'matumbo ake ndi nthenda yosachira nayo.","Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pake pa zaka ziwiri, anatuluka matumbo ake mwa nthenda yake namwalira nazo nthenda zoipa. Ndipo anthu ake sanampserezere zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ake.","Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai."]