bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.71 kB
JSON
["Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu.","Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,","Lankhula ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,","Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense kunyumba yake; pakuti chinthu ichi chifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobowamu.","Ndipo Rehobowamu anakhala m'Yerusalemu, namanga midzi yolimbikiramo m'Yuda.","Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekowa,","ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,","ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,","ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka,","ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo midzi yamalinga ya m'Yuda ndi Benjamini.","Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi chakudya chosungikiratu, ndi mafuta, ndi vinyo.","Ndi m'midzi iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.","Ndipo ansembe ndi Alevi okhala m'Israele lonse anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse.","Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;","nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a anaang'ombe adawapanga.","Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.","Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehobowamu, mwana wa Solomoni zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomoni zaka zitatu.","Ndipo Rehobowamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu mwana wa Yese;","ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu.","Ndi pambuyo pake anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.","Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake ang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana akazi makumi asanu ndi limodzi).","Ndipo Rehobowamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkulu, kalonga mwa abale ake; ndiko kuti adzamlonga ufumu.","Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumidzi yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka."]