bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.34 kB
JSON
["Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yake m'manja a Afilisti.","Anakanthanso Mowabu; ndi Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso.","Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.","Ndipo Davide analanda magaleta ake chikwi chimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magaleta, koma anasungako ofikira magaleta zana limodzi.","Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadadezere mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.","Ndipo Davide anaika asilikali a boma m'Aramu wa Damasiko; ndi Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nazo mphatso. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.","Natenga Davide zikopa zagolide zinali pa anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu.","Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, midzi ya Hadadezere, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomoni anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.","Ndipo pakumva Tou, mfumu ya ku Hamati, kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezere mfumu ya ku Zoba,","anatumiza Hadoramu mwana wake kwa mfumu Davide, kumlonjera ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadadezere, namkantha; pakuti Hadadezere adachita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundumitundu za golide ndi siliva ndi mkuwa.","Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Mowabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleke.","Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu m'Chigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.","Ndipo anaika asilikali a boma m'Edomu; ndi Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.","Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, naweruza anthu ake onse, nawachitira chilungamo.","Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira khamu la nkhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri.","Ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndi Savisa anali mlembi,","ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu."]