UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.8 kB
["Afilisti tsono analimbana nkhondo ndi Israele; ndipo amuna a Israele anathawa pamaso pa Afilisti, nagwa ophedwa pa phiri la Gilibowa.","Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Saulo ndi ana ake, ndi Afilistiwo anawapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.","Ndi nkhondoyi inamkulira Saulo, ndi amauta anampeza; ndipo anatenga nkhawa chifukwa cha amauta.","Pamenepo Saulo anati kwa wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Saulo anatenga lupanga lake, naligwera.","Ndipo pamene wonyamula zida zake anaona kuti Saulo wafa, anagwera nayenso lupanga lake, nafa.","Momwemo anafa Saulo, ndi ana ake atatu; ndi nyumba yake yonse idafa pamodzi.","Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m'chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya midzi yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo.","Ndipo m'mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa pa phiri la Gilibowa.","Ndipo anamvula natenga mutu wake, ndi zida zake, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m'mafano ao ndi mwa anthu.","Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya milungu yao, napachika mutu wake m'nyumba ya Dagoni.","Ndipo onse a Yabesi-Giliyadi, atamva zonse Afilisti adachitira Saulo,","anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.","Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,","osafunsira kwa Yehova; chifukwa chake anamupha, napambutsira ufumu kwa Davide mwana wa Yese."]