UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 4.78 kB
["Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.","Ndipo anati,Yehova ndiye thanthwe langa,ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.","Mulungu wa thanthwe langa,Iye ndidzamkhulupirira;chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa,nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.","Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande;chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.","Pakuti mafunde a imfa anandizinga,mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine.","Zingwe za kumanda zinandizingira;misampha ya imfa inandifikira ine.","M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;ndipo Iye anamva mau anga ali m'Kachisi wake,ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.","Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.Maziko a dziko la kumwamba anasunthika.Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.","M'mphuno mwake munatuluka utsi,ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga;makala anayaka nao.","Anaweramitsa miyambanso, natsika;ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.","Ndipo Iye anaberekeka pa kerubi nauluka;inde anaoneka pa mapiko a mphepo.","Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye,kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga.","Cheza cha pamaso pakemakala a moto anayaka.","Yehova anagunda kumwamba;ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ake.","Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza;mphezi, nawaopsa.","Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka,maziko a dziko anaonekera poyera,ndi mtonzo wa Yehova,ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.","Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga;Iye ananditulutsa m'madzi aakulu.","Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,kwa iwo akudana ndi ine;pakuti anandiposa mphamvu.","Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;koma Yehova anali mchirikizo wanga.","Iye ananditulutsanso ku malo akulu;Iye anandipulumutsa,chifukwa akondwera ndi ine.","Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho.","Pakuti ndinasunga njira za Yehova,osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.","Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga;ndipo za malemba ake, sindinawapatukira.","Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye,ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga.","Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;monga mwa kuyera kwanga pamaso pake.","Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo,ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro.","Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.","Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.","Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.","Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.","Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro;mau a Yehova anayesedwa;Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.","Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?","Mulungu ndiye linga langa lamphamvu;ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake.","Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala;nandiika pa misanje yanga.","Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.","Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.","Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,ndi mapazi anga sanaterereke.","Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga;ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.","Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka,inde anagwa pansi pa mapazi anga.","Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo;munandigonjetsera akundiukira.","Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.","Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe.","Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko,ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.","Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;Anthu amene sindinawadziwa adzanditumikira ine.","Alendo adzandigonjera ine,pakumva za ine, adzandimvera pomwepo.","Alendo adzafota,nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.","Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa;","inde Mulungu wakundibwezera chilango ine,ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.","Amene anditulutsa kwa adani anga;inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.","Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.","Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu;naonetsera chifundo wodzozedwa wake,kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse."]