bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 4.17 kB
JSON
["Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.","Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.","Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.","Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.","Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.","Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pamadzi, lilekanitse madzi ndi madzi.","Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi anali pamwamba pa thambolo; ndipo kunatero.","Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.","Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.","Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.","Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, pa dziko lapansi: ndipo kunatero.","Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.","Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu.","Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;","Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi: ndipo kunatero.","Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.","Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi.","Nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.","Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachinai.","Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga.","Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.","Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke pa dziko lapansi.","Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu.","Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.","Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.","Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.","Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.","Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.","Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:","ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.","Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi."]